Psalms 132

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

1Inu Yehova, kumbukirani Davide
ndi mavuto onse anapirira.

2Iye analumbira kwa Yehova
ndi kulonjeza kwa Wamphamvu wa Yakobo kuti,
3“Sindidzalowa mʼnyumba mwanga
kapena kugona pa bedi langa:
4sindidzalola kuti maso anga agone,
kapena zikope zanga ziwodzere,
5mpaka nditamupezera malo Yehova,
malo okhala a Wamphamvu wa Yakobo.”

6Zoonadi, tinamva za Bokosi la Chipangano ku Efurata,
tinalipeza mʼminda ya ku Yaara:
7“Tiyeni tipite ku malo ake okhalamo;
tiyeni tikamulambire pa mapazi ake.
8‘Dzukani Yehova, ndipo bwerani ku malo anu opumulira,
Inuyo ndi Bokosi la Chipangano limene limafanizira mphamvu zanu.
9Ansembe anu avekedwe chilungamo;
anthu anu oyera mtima ayimbe nyimbo mwachimwemwe.’ ”

10Chifukwa cha Davide mtumiki wanu,
musakane wodzozedwa wanu.

11Yehova analumbira kwa Davide,
lumbiro lotsimikizika kuti Iye sadzasintha:
“Mmodzi wa ana ako
ndidzamuyika pa mpando waufumu;
12ngati ana ako azisunga pangano langa
ndi malamulo amene ndiwaphunzitsa,
pamenepo ana awo adzakhala pa mpando
wako waufumu kwamuyaya ndi muyaya.”

13Pakuti Yehova wasankha Ziyoni,
Iye wakhumba kuti akhale malo ake okhalamo:
14“Awa ndi malo anga opumapo ku nthawi za nthawi;
ndidzakhala pano pa mpando waufumu, pakuti ndakhumba zimenezi.
15Ndidzadalitsa mzindawu ndi zinthu zambiri;
anthu ake osauka ndidzawakhutitsa ndi chakudya.
16Ndidzaveka ansembe ake chipulumutso,
ndipo anthu ake oyera mtima adzayimba nthawi zonse nyimbo zachimwemwe.

17“Pano ndidzachulukitsa mphamvu za Davide
ndi kuyikapo nyale ya wodzozedwa wanga.
18Ndidzaveka adani ake manyazi,
koma chipewa chaufumu pamutu pake chidzakhala chowala.”
Copyright information for NyaCCL